Kupititsa patsogolo kupezeka kwa Mbewu ndi Chakudya mMalawi: Gawo lomwe Nyunda za mbewu zaku muzi ('Improving Seed and Food Security in Malawi: The Role of Community Seed Banks')
FNI Policy Brief 3/2022. Lysaker, Fridtjof Nansen Institute, June 2022, 9 p. Translation into Chichewa of the English original.
FNI Policy Brief 3/2022. Lysaker, Fridtjof Nansen Institute, June 2022, 9 p. Translation into Chichewa of the English original.
Mfundo Zikuluzikulu:
- Alimi ang’ono ang’ono amadalira ulimi wa mbewu zosiyanasiyana pogwiritsa ntchito mbewu zamakolo. Kasinthasintha ameneyu akuwathandizila mu nthawi yakusintha kwa nyengo komanso kupeza chakudya chofunikira mthupi lawo.
- Ngakhale zili choncho mbewu za makolozo zikupitilira kusowa komanso madera ena zinatheratu.
- Kasinthasintha wa mbewu kuno ku Malawi anachepa kamba kamalamulo okhuza mbeu omwe sakusimikiza kwambiri zakufunika kwa mbeu za lokolo pothandizila kuthetsa njala komaso kuthandizila popeza magulu onse achakudya.
- Nyumba za mbewu za kumudzi zimathandizila kapezekedwe ka mbewu za makolo ndi kasamalidwe ka chakudya pokhala ngati likulu loyambitsanso kasinthasintha wa mbewu za makolo.
- Kuonjezera nyumba za mbewu za kumudzi ndi njira imodzi yofunikira kupitisa patsogolo kupezeka kwa mbewu ndi chakudya kwa alimi ang’onoang’ono M’malawi.